Verse 1
Mam’mawa, masana, madzulo,
Simusintha muli yemweyo
Khutu lanu silogontha
Kuti mungalephere kundimva
Mkono wanu siwawufupi
Kuti mulephere kukhudza
Maso anu si akhungu
Kuti mulephere kupenya
Pali timilungu tina
tomwe anthu amapembedza
Maso ato ndi akhungu
Sitingathe kuwapenya
Tili ndi makutu inde
Sitingathe ku wamva
Tili ndi manja inde sitingathe kuwa pulumutsa
Chorus
Sindi dzapembedza
milungu ina
Koma inu Mulungu wamoyo
Verse 2
Mene mumkalenga dzikoli
Munali napo pokhala
Mene mumkalenga kumwamba malo anu analipo
Mene mkalenga nyanja
Mene mumkalenga mapiri
Mene mumkalenga Munthu
Munalenga ndi mawu anu
Munati tilenge Munthu
Nchifaniziro chathu
Chifanizo cha inu
Tate, mwana ndi Mzimu woyera
Chorus
Sindi dzapembedza
milungu ina
Koma inu Mulungu wamoyo