Verse 1
Ndina sochela kutali,
Ine ndinadya ndi nguluwe,
Moyo wanga ine unatayika,
Koma Ambuye munandigwira dzanja.
Chorus
Mwayenela,
Mwayenela,
Mwayenela,
Ndinu chipulumutso changa.
Verse 2
Satana amakondwa,
Akandiona kuti ndagwa,
Popeza amadziwa
Kuti wagonjetsa,
Kwake ndi kuba, kupha ndi kuwononga.
Chorus
Mwayenela,
Mwayenela,
Mwayenela,
Ndinu chipulumutso changa.