Chorus
Ndiwe Odala Odala Odala Odala x 4
Verse 1
Kaya waphinjika usataye mtima yesu wamoyo ali pa mbari pako
Nyengo zathina usandaure itana mbuyeyesu adzakuyankha
Wasowa chakudya usandaure kuti udzadya chan itana yesu
Ukusowa mwana usandaure kumbuka Hanna nae Nyengo zake
Ukusowa banja lowa nchipinda chako pinda bondo lako ambuye akumva
Ndiwe lova pemphera Sala kudya Mulungu omva tseli adzakuyankha
Kumbukira sachedwa safulumira mu nthawi yoyikika iye adzayankha
Tikapemphera kulibe Nyengo zomwe zingamulake iye adzayankha.
Chorus
Verse 2
Dziko limanyoza ili dziko limatodza ili dziko limaweluza
Koma Kumbukira chouluka chingauluke imakwana nthawi ndipo chimatera
M’dima ukure bwanji kunja kungade bwanji koma kumaera iwe dikilabe
Mavuto achuluke osatenga chingwe kuchosa moyo wako iwe pempherabe
Maso a Yehova amaona ponse khutu lake silogotha iwe pempherabe
Pamene wathedwa mzeru wasowa mtengo ogwira chisomo chimaoneka iwe pempherabe
Analonjeza mdalitso kwa onse okhulupilira omwe ndi ana ake adzawadalitsa
Uuuuuuuuuuuuuuuuu
Chorus