Home Lyrics Judith Longwe _ Tasakaniza Milungu _Lyrics

Judith Longwe _ Tasakaniza Milungu _Lyrics

by Harris Msosa
803 views

Verse 1.

Pachiyambi akuti
Panali mawu ndipo
Mawuwo anali iye mulungu zinthu zonse zinadza kamba ka iye ndipo
Moyowu unalengedwa ndi iye
Anachita izi Kuti tidziwe Kuti ndiyekhayo watipatsa moyo panalibe wothandiza
Naye sadanene Kuti
Tikapsinjika ndi nyengo tifunefune
Nzeru Kwa milungu ina wanenetsa adzatikankha chifukwa safuna
Kumusakaniza

Chorus…

Wonani tchimo ili
Lakula
Wonani yehova inu
Wakwiya tasakaniza
Milungu yehova inu
Wakwiya tasakaniza milungu kumwamba
Inu kwakwiya

Verse 2…

Potilenga mwini anadziwa
Za moyo wathu adzathana nazo
Iye palibe chomwe
Chingamukanike
Tisadalire wongowona zakuthupi takhulupirira wosatilenga takaikira
Wotilenga timapeza
Phindu Kwa milungu
Ina tikafuna banja
Tipita Kwa milungu
Ina zikavuta yawe
Imani nane ndichifukwa chake
Vuto silitha tasakaniza milungu
Yehova wakwiyaaa

Chorus…

Wonani tchimo ili
Lakula
Wonani yehova inu
Wakwiya tasakaniza
Milungu yehova inu
Wakwiya tasakaniza
Milungu kumwamba
Inu kwakwiya

kuwalagospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel music. For inquiries contact these numbers 0888 069 117/0983 592 032 or info@kuwalagospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media