Chorus
Pamene mukapanga za ine
Ine ndikupanga za Mulungu
Mulungu akupanga zaine kukonderedwa kokhakokha
Ndikonda mmene amandikondera
Nyengo zanga amazipangira handle
Nkhondo zanga amazimenyeraa chipambano chokhachoka
Verse 1
Kuchoka tsiku lomwe ndinadziwa
Kuti mwini nkhondo alipo
Sindimadandaula
Ndidziwa chipambano chilipo
Andimenyera nkhondo mmalo mwanga ine ndili chetee zosamvetsetseka
Mpaka adani chete chete
Ndimakhala ndili pa easy
Nthawi yodandaula ndilibe
Ndimangomva zothaitha kuti adani anga agonja
Back to chorus
Melody
Verse 2
Monga momwe achitila mwana, okonderedwa ndi bambo ake
Akamenyedwa ndi azinzake, amakanenana kwa bambo akewo
Inenso chimodzimodzi, ndilibe nthawi yolimbana nanu
Olimbana nane alimbana ndabambo angawo
Olimbana nane alimbana naye
Ondikumbira dzenje adzagwera ekha
Oboola mpanda njoka idzamuluma ekha
Back to chorus
Melody
Back to chorus till end