Yobu Bazale Kachitenji from Mponela Boma la Dowa.Mbiri yamoyo wake kufika lelo ndichisomo cha yahwe.Ku banja lakwawo ndi mwana wa number 5 kubadwa koma anakula moyo ovutika, school yake analekezera form 1 chifukwa chosowa chithandizo.
Wakhala moyo ovutika ,matenda mkati omwe amati matenda akugwa. Anadwala zaka zitatu koma Mulungu anasitha nyengo tikunena pano amapanga business ya ma herbal.Pano iye ndi oyimba ozidalila payekha makolo ake,azibale ake and all the family amadalila iyeyo.
Akamaimba nyimbo zake samangoyimba kusangalatsidwa ayi koma amayimba pofuna kufalitsa uthenga wabwino ndikulimbikitsa anthu ena omwe akudutsa munyengo zonse zolimba ngati fupa la mkango kuti pamene wina akumumva akudutsa munyengo zonse zowawa asataye mtima Mulungu amasamala ,amatothoza nyengo umboni alinawo anawonera pa iye mwini nyengo zake zatothola yahwe Ndiye mwini wazonse.
2018 anatulutsa Chimbale choyamba chotchedwa WASINTHA NYENGO ZANGA nyimbo iyi imamukumbutsa nyengo zake zowawa komabe samataya chiyembekezo amadziwa zikudikila thawi ndi nyengo.
Pano anayamba kutulutsa nyimbo zachimbale chachiwili chomwe sichikudziwika kuti chidzatchedwa chani mutu wake chifukwa muchimbale chimenechi muli nyimbo 4 .
Nyimbo yoyamba yotchedwa
1 .LINGA LANGA
2.ZIYENDELENI
3.MFUMU YA MAMFUMU WORSHIP GOSPEL
4.MKAWONANENAYE YESU WAMOYO.
Pa Nyimbo izi yekha akamamvera amadalitsika nazo chifukwa cha nyengo zolimba zomwe iye anadutsamo ndipo samkadziwa kuti phazi lake nsapato mkudzavalapo , nyumba ya self contained mkudzakhalamo, njinga ya moto mkudzakhala nayo.