Home Artist Biography THOM HENRY – BIOGRAPHY

THOM HENRY – BIOGRAPHY

by Kuwala Gospel Music
233 views

Thom Henry ndi mwana oyamba kubadwa mubanja la mayi ndi bambo Henry ndipo amakhala mu boma la Blantyre.Anabadwa chaka cha 1991 ku Chikowa hospital,Traditional Athority Kunthembwe ndipo kunkhani ya maphunziro ake anapangira ku Dzunga Primary School from standard 1 mpaka 8, from there anapita pa Chikuli SDCC Secondary School form 1 mpaka 4 koma kamba ka mavuto azachuma sanathe kupita nayo school patali.

Kumbali ya moyo wake wa uzimu anayamba kupemphela ali wamng’ono ndimakolo ake koma kamba koti bambo ake ndi Raster Man mayi ake ndi a Mtopiya Zayoni ngati mwana zinamuvuta kupanga chisankho kotsatila m’modzi mwa kholo lake kumapita kopemphela ndipo izi zinamupangitsa kukayamba mpingo wa The Revalation Church of Jesus Christ (International) mu chaka cha 2011 pomwenso anayamba kwaya ndikupatsidwa udindo wa vice Choir master ndipo kwayai inatulutsapo DVD tittle Tili ndi Mwai mu chaka cha 2013 yomwe inatuluka mu 2014 koma kamba ka mbali yake ya moyo wathupi anapanga chisankho chopita ku South africa, Capetown kumapeto kwa 2013 komwe anakayamba kusaka maganyu.Koma izi ngakhale zinali choncho sanasiye kutumikila Ambuye kudzela m’mayimbidwe mwakuti mu chaka cha 2019 anatulutsa album yake title: Mwandigometsa nyimbo zongomvela zomwe zinalandilidwako ndi anthu ambiri,ali mkati mokuti apange promote album imeneyi komanso kuti ajambule ma videos ndikupanga launch mu chaka cha 2020 ndipomwe anakumana ndi vuto la matenda a Corona choncho ma pulani onse analepheleka komabe poti kuyimba kwa iye amautenga ngati utumiki sanataye mtima konse anayambanso kujambula nyimbo zina( album ina nyimbo zoonela) title Udzigulile Moyo yomwe ikuyembekezeka kutuluka mu chaka cha 2024 pa 13 October as a Launch.Kumpingo komwe iye amapemphera ndi General Secretary.

You may also like

Leave a Comment

kuwalagospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel music. For inquiries contact these numbers 0888 069 117/0983 592 032 or info@kuwalagospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media