Home Artist Biography POSTAN NKHOMA – BIOGRAPHY

POSTAN NKHOMA – BIOGRAPHY

by Kuwala Gospel Music
365 views

Postan Nkhoma anabadwa pa 02 May 1995 pa Ngoni Health Center ku Lilongwe,Traditional Authority Mtema m’mudzi wa Sulumbwa.Ndipo ndi mwana oyamba kubadwa pa ana 6, currently alipo 5,amuna okhaokha,wamkazi anamwalira mu chaka cha 2008.

Atangobadwa adapatsidwa dzina lakuti Chipiliro chifukwa chakuti iye anabadwa nthawi yomwe makolo ake anali atatha zilumika ziwiri popanda kukhala ndi mwana.

Ndipo anachita maphunziro ake a primary school pa Chimphepo Full Primary School kenako mu chaka Cha 2012 anasankhidwa ndikukapitiliza maphunziro ake aku secondary pa Mtemambalame Community Day Secondary ndipo ali ndi certificate ya Malawi School Certificate of Education.

Mayitanidwe amayimbidwe adamufikira ali ndi zaka zisanu ndi zinai (14) koma kufika pa air anayamba pa 30 may 2023 pomwe adatulutsa album yotchedwa Kanthawi yomwe muli nyimbo 10 monga:

1 Amawala
2 kanthawi
3 Udzakondwa
4 Timtumikire
5 Tidzauka
6 Samasintha
7 Akudziwa
8 Nangula
9 Chikondi chake
10 ndikuyamika

Ndipo anadalitsika ndi banja komanso mwana wamamuna dzina lake Joshua.Dzina lomwe akudziwika nalo mu music industry ndi Postan Nkhoma.Postan ndi dzina la abambo ake pomwe Nkhoma ndi la mfunda wawo.

You may also like

Leave a Comment

kuwalagospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel music. For inquiries contact these numbers 0888 069 117/0983 592 032 or info@kuwalagospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media