Home Artist Biography Litah Lubano Nine – Biography

Litah Lubano Nine – Biography

by Harris Msosa
578 views

Litah Lubano Nine amachokera Ku Blantyre m’dera la chilaweni mudzi mwa mwanzanga T/A Machinjiri amakhala Ku south Africa dera lotchedwa Germiston.Kwawo anabadwa ana 4 ndipo iyeyo ndi oyamba kubadwa ndipo anabadwa chaka cha 1987 pa 12 April.

Anayamba kuimba ali wachichepele koma amaimba kwaya ya pa Church kufikira atakula kuyamba kumutumikira Mulungu mu chaka cha 2016 anadwala kwambiri samadya, samayenda for the first time moyo Wake kudwala kotele ndipo ali m’kati modwalamo Mulungu anamuuza kuti wamuchilitsa ndipo kumuchilitsako akufuna kuti amutumikire ndipo mam’mawa m’mene kunacha anaziona kuti sakudwalanso ndipo anayenda, anadya zimene zinadabwitsa anthu kwambiri chifukwa palibe amadziwa kuti iyeyo angayendenso ndipo anayamba kutumikira Mulungu munjira zosiyanasiyana kufikira chaka cha 2022 chimene Mulungu anamuyakhulanso kuti akuyenera kumutumikira kudzera mukuyimba. mukamamvera nyimbo zake akumamuyamika Mulungu kwambiri chifukwa akadapanda kumuchilitsa ndiye kuti iyeyo bwezi kulibe.

You may also like

Leave a Comment

kuwalagospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel music. For inquiries contact these numbers 0888 069 117/0983 592 032 or info@kuwalagospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media