Home Artist Biography HAWA CHITENJE MAKOTOLA – BIOGRAPHY

HAWA CHITENJE MAKOTOLA – BIOGRAPHY

by Kuwala Gospel Music
99 views

Hawa Chitenje Makotola anabadwila ku Nkhotakota kukula kwake wakulila moyenda cfk bambo ake anali driver wa ma therekita amizimbe kalelo.Hawa bambo ake ndi akwachibwana m’boma la Machinga M’mudzi mwa Chombe T/A Kaporoma ndipo mayi ake a Hawa kumudzi kwawo ndi m’boma la Chikwawa ku Dembo m’mudzi mwa a Liwonde mfumu yaikulu Mpokonyola T/A Katunga.

Mubanja mwawo anabadwa ana 9, omwalila awili ndipo otsala 7, akazi atatu, amuna 4 ndipo Hawa ndiwanamba 6 kubadwa ndipo kufika lero ali ndi kholo limodzi la bambo lokha pakuti mayi ake anamwalila pa 2 December 2023.

Hawa ndi oyimba nyimbo za uzimu ndipo luso loyimba anayamba ali mwana,alimwana amkayimba kwaya mu mpingo wa Babtist mu kwaya yomwe imkatchedwa Madalitso Choir munthawi imeneyo amakwanitsa kutsogolela nyimbo pa gulu la amzake. Atakula amayimbabe ma choir kumvano ndikumatsogolelaso nyimbo kufikila mu chaka cha 2021 anayamba kupeka nyimbo zake payekha komanso kuyamba kujambula nyimbozo ndipo atamaliza kujambula anapanga launch ya chimbale chake choyamba chomwe mutu wake ndi Tidzazindikila bwino pa tsogolo mwachidule amati Patsogolo Album umu ndimu chaka cha 2022 pa 31 December ndipo kufika lelo Hawa Chitenje ali ndi album imodzi ndi nyimbo 4,ma video 13 ndi imodzi yomwe sanajambule video.

Hawa Chitenje Makotola ndi okwatiwa ali ndi ana 4, akazi atatu, wamamuna m’modzi ndipo panopa Hawa akukhalila m’boma la Chikwawa kwa Ngabu ku banja.

You may also like

Leave a Comment

kuwalagospelmusic.com is a Christian music website with all Malawian gospel music. For inquiries contact these numbers 0888 069 117/0983 592 032 or info@kuwalagospelmusic.com

All Rights Reserved – Designed and Developed by Kay Dee Media