Bignna Phiri anabadwa komanso kukulira ku Nkhata Bay Chintheche m’mudzi wa G.V Vuwanga ndipo anabadwa pa 4 March 1984 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana okwana 4 koma adatsala amoyo atatu m’modzi adamwalira ndipo iye ndi wa number 4 pobadwa.
Kukamba zamayimbidwe Bignna wayimbapo Mdyaka Voice Choir ya ku Chintheche ndipo mu 2013 anayimbanso mu choir ya Golden Voice ndipo pano akuyimbanso mu choir ya Durban Chipulumutso ya ku Embo CAP Vestry. Kuyimba pa yekha anayamba mu 2018 pomwe anatulutsa nyimbo yotchedwa Mwawanthu Akuchiuta imene inali muchiyankhuro cha chi tonga ndipo ma producer amene pano akugwira nawo ntchito ndi Maxy F Nampinga mwini wake wa Passion Media ndi Peter Michael Pemba.