Elizabeth Beatrice Kadyamphungo (LIZBK) anabadwa komanso kukulira ku Zomba kwa a Jokala, Male village T/A Malemia. Anabadwa pa 4 April,1982 ndipo mu banja mwawo anabadwa ana 11 ndipo iye ndi wa number 10 (pomwe pakalipano anatsala 7 mubanjali).
Atabadwa anapatsidwa dzinaloti Beatrice, ndipo atabatidzidwa, anadalitsidwa ndidzina loti Elizabeth lomwe pachidule ndi Liz, pamene full ili Elizabeth (Liz) Beatrice (B) Kadyamphungo (K)=LizBk.
Maimbidwe ake anayamba ali wachichepere koma kuimba payekha anayamba 2012 pomwe wakhala akuimba ndi maband osiyanasiyana mpaka kuyamba kutulutsa nyimbo zake muchamba cha reggae. LIZBK anayamba kuimbira Ambuye(gospel) muchaka cha 2018 pomwe anatulutsa album yake yotchedwa Khungu.Kuchokera pamenepo wakhala akutulutsa ma album ndi ma singles ake muzamba monga reggae, afro,amapiano ndi zina zosiyanasiyana.LIZBK ndimzimayi wa ana atatu anyamata awiri komanso mtsikana m’modzi.
LIZBK yemwe wadziwika kwambiri ku nyimbo za reggae komanso ndi amapiano ndi nyimbo yoti Wayaka Moto, palibe chida ndi ina yatsopano yotchedwa Nanga kwanuko bwa?LizBk pano adakali ndi project ya nyimbo za praise and worship zomwe zituluke mwezi oyambilira wa 2024.
LIZBK ndimzimayi wa business zosiyanasiyana komanso ndimembala wampingo wa Assemblies of God.LIZBK ndi member wa MUM kwazaka komanso COSOMA.